-
Deuteronomo 1:16, 17Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Pa nthawi imeneyo ndinauza oweruza anu kuti, ‘Mukamaweruza mlandu pakati pa abale anu, muziweruza mwachilungamo+ pakati pa munthu ndi mʼbale wake kapena ndi mlendo.+ 17 Musamakondere poweruza mlandu.+ Munthu wamba ndi munthu wolemekezeka, onse muziwamvetsera chimodzimodzi.+ Musamaope anthu+ chifukwa mukuweruzira Mulungu+ ndipo ngati mlandu wakuvutani muzibwera nawo kwa ine kuti ndiumve.’+
-