2 Mbiri 6:36 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 36 Anthu anu akakuchimwirani (popeza palibe munthu amene sachimwa)+ inu nʼkuwakwiyira kwambiri ndiponso kuwapereka kwa adani, adani awowo nʼkuwatenga kupita nawo kudziko lakutali kapena lapafupi,+ Salimo 51:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Taonani! Ndinabadwa ndili wochimwa,Ndipo ndine wochimwa kuchokera pamene mayi anga anatenga pakati panga.+ Aroma 3:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Popeza anthu onse ndi ochimwa ndipo amalephera kusonyeza bwinobwino ulemerero wa Mulungu.+ 1 Yohane 1:8 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 8 Tikamanena kuti, “Tilibe uchimo,” ndiye kuti tikudzinamiza+ ndipo mumtima mwathu mulibe choonadi.
36 Anthu anu akakuchimwirani (popeza palibe munthu amene sachimwa)+ inu nʼkuwakwiyira kwambiri ndiponso kuwapereka kwa adani, adani awowo nʼkuwatenga kupita nawo kudziko lakutali kapena lapafupi,+
5 Taonani! Ndinabadwa ndili wochimwa,Ndipo ndine wochimwa kuchokera pamene mayi anga anatenga pakati panga.+