-
Mlaliki 5:18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Chinthu chabwino kwambiri ndiponso choyenera chimene ine ndaona nʼchakuti: Munthu ayenera kudya, kumwa ndi kusangalala+ chifukwa cha ntchito yake yonse yovuta imene amaigwira mwakhama padziko lapansi pano, kwa masiku ochepa a moyo wake amene Mulungu woona wamupatsa. Chifukwa imeneyo ndi mphoto yake.*+
-
-
Mlaliki 9:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Sangalala ndi moyo limodzi ndi mkazi wako amene umamukonda+ masiku onse a moyo wako wachabechabe, amene Mulungu wakupatsa padziko lapansi pano. Usangalale masiku ako onse achabechabe, chifukwa imeneyi ndi mphoto imene* ukuyenera kulandira pa moyo wako komanso pa ntchito yovuta imene ukuigwira mwakhama padziko lapansi pano.+
-