46 Lero Yehova akupereka mʼmanja mwanga,+ ndipo ndikupha nʼkukudula mutu. Lero ndipereka mitembo ya asilikali amʼmisasa ya Afilisiti kwa mbalame zamumlengalenga ndi kwa zilombo zakutchire. Anthu onse apadziko lapansi adzadziwa kuti Aisiraeli ali ndi Mulungu.+