Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Samueli 7:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 8 Tsopano mtumiki wanga Davide ukamuuze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Ine ndinakutenga kubusa kumene unkaweta nkhosa+ kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga.+

  • 2 Samueli 7:16
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Nyumba yako ndi ufumu wako zidzakhalapobe mpaka kalekale. Mpando wako wachifumu udzakhazikika mpaka kalekale.”’”+

  • 2 Samueli 23:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  5 Kodi nyumba yanga siili choncho kwa Mulungu?

      Chifukwa wachita nane pangano lomwe lidzakhalapo mpaka kalekale,+

      Analikonza bwino ndipo ndi lotetezeka.

      Chifukwa ndi chipulumutso changa ndipo limandisangalatsa,

      Chimenechi ndiye chifukwa chake amakulitsa panganoli.+

  • Salimo 89:28, 29
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Ndidzapitiriza kumusonyeza chikondi changa chokhulupirika mpaka kalekale,+

      Ndipo pangano limene ndinachita naye silidzaphwanyidwa.+

      29 Ndidzachititsa kuti mbadwa* zake zidzakhalepo kwamuyaya,

      Ndipo ndidzachititsa kuti mpando wake wachifumu udzakhalepo mpaka kalekale ngati kumwamba.+

  • Yeremiya 33:25, 26
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 25 Yehova wanena kuti, ‘Mofanana ndi mmene ndinakhazikitsira pangano langa loti kukhale masana ndi usiku,+ malamulo akumwamba ndi dziko lapansi,+ 26 sindidzakananso mbadwa* za Yakobo ndi za Davide mtumiki wanga, kuti pakati pa mbadwa* zake ndisatengepo olamulira ana a Abulahamu,* Isaki ndi Yakobo. Chifukwa ndidzasonkhanitsa anthu onse amene anatengedwa kupita kudziko lina+ ndipo ndidzawamvera chisoni.’”+

  • Machitidwe 13:34
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 34 Ndipo mfundo yakuti iye anamuukitsa ndipo sangabwererenso kuthupi limene limavunda,* anaifotokoza chonchi: ‘Ine ndidzakusonyezani anthu inu chikondi chokhulupirika chimene ndinalonjeza Davide. Lonjezo limeneli ndi lodalirika.’+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena