-
1 Mbiri 17:7-10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Tsopano mtumiki wanga Davide ukamuuze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti: “Ine ndinakutenga kubusa kumene unkaweta nkhosa kuti ukhale mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli.+ 8 Ine ndidzakhala nawe kulikonse kumene ungapite+ ndipo ndidzagonjetsa adani ako onse pamaso pako.+ Ndidzachititsa kuti dzina lako lidziwike ngati mmene zimakhalira ndi anthu otchuka mʼdzikoli.+ 9 Anthu anga Aisiraeli ndidzawasankhira malo nʼkuwakhazika pamalowo. Iwo adzakhala pamenepo ndipo sadzasokonezedwanso. Anthu oipa sadzawaponderezanso ngati mmene ankachitira kale,+ 10 pa nthawi imene ndinasankha oweruza kuti azitsogolera anthu anga Aisiraeli.+ Ndipo ndidzagonjetsa adani ako onse.+ Kuwonjezera pamenepo, ndikukuuza kuti: ‘Yehova adzakumangira nyumba.’*
-
-
1 Mbiri 28:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Komabe, mʼnyumba yonse ya bambo anga Yehova Mulungu wa Isiraeli anasankha ineyo kuti ndikhale mfumu ya Isiraeli mpaka kalekale,+ chifukwa anasankha Yuda kuti akhale mtsogoleri.+ Mʼnyumba ya Yuda anasankhamo nyumba ya bambo anga.+ Pa ana a bambo anga anavomereza ineyo kuti ndikhale mfumu ya Aisiraeli onse.+
-