-
Mateyu 13:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Ulosi wa Yesaya ukukwaniritsidwa pa iwowa. Ulosiwo umanena kuti: ‘Kumva mudzamva ndithu, koma simudzazindikira tanthauzo lake. Kuyangʼana mudzangʼana ndithu, koma simudzaona chilichonse.+ 15 Chifukwa anthu awa aumitsa mitima yawo ndipo amva ndi makutu awo koma osalabadira. Atseka maso awo kuti asaone ndi maso awo komanso kuti asamve ndi makutu awo nʼkuzindikira tanthauzo lake mʼmitima yawo kenako nʼkutembenuka kuti ine ndiwachiritse.’+
-
-
Luka 8:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Koma ophunzira ake anamufunsa tanthauzo la fanizo limeneli.+ 10 Iye anati: “Inu mwapatsidwa mwayi woti mumvetse zinsinsi zopatulika za Ufumu wa Mulungu. Koma kwa enawo, zonse ndi mafanizo okhaokha.+ Izi zili choncho kuti kuyangʼana aziyangʼana ndithu, koma kukhale kopanda phindu, kumvanso azimva ndithu, koma asamamvetse zimene zikunenedwa.+
-
-
Machitidwe 28:25-27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Choncho, popeza ankatsutsana, anayamba kuchoka. Koma Paulo ananena mawu awa:
“Mzimu woyera unanena zoona kwa makolo anu kudzera mwa Yesaya mneneri. 26 Mzimuwo unati, ‘Pita ukauze anthu awa kuti: “Kumva mudzamva ndithu, koma simudzazindikira. Kuyangʼana mudzayangʼana ndithu, koma simudzaona chilichonse.+ 27 Chifukwa anthu awa aumitsa mitima yawo ndipo amva ndi makutu awo, koma osalabadira. Atseka maso awo kuti asaone ndi maso awo komanso kuti asamve ndi makutu awo nʼkumvetsa tanthauzo lake mʼmitima yawo, kenako nʼkutembenuka kuti ine ndiwachiritse.”’+
-