Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 2:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Mulungu adzaweruza anthu a mitundu yosiyanasiyana

      Ndipo adzakonza zinthu zimene ndi zolakwika pakati pawo.

      Iwo adzasula malupanga awo kuti akhale makasu a pulawo,

      Ndipo mikondo yawo adzaisula kuti ikhale zida zosadzira mitengo.+

      Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake,

      Ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo.+

  • Yesaya 35:9
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  9 Mmenemo simudzakhala mkango

      Ndipo nyama zolusa zakutchire sizidzafikamo.

      Nyama zotere sizidzapezekamo.+

      Anthu okhawo amene anagulidwanso ndi amene adzayende mumsewuwo.+

  • Yesaya 60:18
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 18 Mʼdziko lako simudzamvekanso zachiwawa

      Mʼdziko lako simudzakhalanso kusakaza kapena kuwononga.+

      Mipanda yako udzaitcha Chipulumutso+ ndipo mageti ako udzawatcha Tamanda.

  • Mika 4:4
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  4 Aliyense adzakhala pansi pa mtengo wake wa mpesa ndi mtengo wake wa mkuyu,+

      Ndipo sipadzakhala wowaopseza,+

      Chifukwa Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena zimenezi.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena