Yesaya 51:3 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 3 Chifukwa Yehova adzatonthoza Ziyoni.+ Iye adzatonthoza malo ake onse amene anawonongedwa.+Adzachititsa chipululu chake kukhala ngati Edeni+Ndipo dera lake lachipululu lidzakhala ngati munda wa Yehova.+ Mwa iye mudzakhala kusangalala ndi kukondwera,Kuyamikira ndi kuimba nyimbo zosangalatsa.+ Yesaya 56:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Nawonso ndidzawabweretsa kuphiri langa loyera+Ndipo ndidzawachititsa kuti asangalale mʼnyumba yanga yopemphereramo. Nsembe zawo zopsereza zathunthu ndi nsembe zawo zina ndidzazilandira paguwa langa lansembe. Chifukwa nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.”+ Yesaya 65:25 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 25 Mmbulu ndi mwana wa nkhosa zidzadyera pamodzi,Mkango udzadya udzu ngati ngʼombe yamphongo,+Ndipo chakudya cha njoka chidzakhala fumbi. Zimenezi sizidzapweteka aliyense kapena kuwononga chilichonse mʼphiri langa lonse loyera,”+ akutero Yehova.
3 Chifukwa Yehova adzatonthoza Ziyoni.+ Iye adzatonthoza malo ake onse amene anawonongedwa.+Adzachititsa chipululu chake kukhala ngati Edeni+Ndipo dera lake lachipululu lidzakhala ngati munda wa Yehova.+ Mwa iye mudzakhala kusangalala ndi kukondwera,Kuyamikira ndi kuimba nyimbo zosangalatsa.+
7 Nawonso ndidzawabweretsa kuphiri langa loyera+Ndipo ndidzawachititsa kuti asangalale mʼnyumba yanga yopemphereramo. Nsembe zawo zopsereza zathunthu ndi nsembe zawo zina ndidzazilandira paguwa langa lansembe. Chifukwa nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu a mitundu yonse.”+
25 Mmbulu ndi mwana wa nkhosa zidzadyera pamodzi,Mkango udzadya udzu ngati ngʼombe yamphongo,+Ndipo chakudya cha njoka chidzakhala fumbi. Zimenezi sizidzapweteka aliyense kapena kuwononga chilichonse mʼphiri langa lonse loyera,”+ akutero Yehova.