6 Yehova wanena kuti,
‘“Chifukwa chakuti Gaza+ wandigalukira mobwerezabwereza, sindidzamusinthira chigamulo changa.
Chifukwa anatenga anthu onse ogwidwa ukapolo+ nʼkuwapereka ku Edomu.
7 Ndidzatumiza moto pampanda wa Gaza,+
Ndipo udzawotcheratu nsanja zake zolimba.
8 Ndidzapha anthu a ku Asidodi,+
Komanso wolamulira wa ku Asikeloni.+
Ndidzalanga Ekironi,+
Ndipo ndidzafafaniza Afilisiti otsala,”+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’