-
Chivumbulutso 22:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
22 Ndipo anandionetsa mtsinje wa madzi a moyo,+ oyera ngati mwala wonyezimira wa kulusitalo, ukuyenda kuchokera kumpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa.+ 2 Mtsinjewo unadutsa pakati pa msewu waukulu wamumzindawo. Kumbali zonse ziwiri za mtsinjewo kunali mitengo ya moyo imene inkabereka zipatso zokolola maulendo 12, ndipo inkabereka zipatso mwezi uliwonse. Masamba a mitengoyo anali ochiritsira mitundu ya anthu.+
-