Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Yesaya 4:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 Tsiku limenelo, chinthu chimene Yehova adzachiphukitse chidzakhala chokongola komanso chaulemerero. Zipatso za mʼdzikolo zidzakhala zonyaditsa ndi zokongola kwa Aisiraeli amene adzapulumuke.+

  • Yesaya 27:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Mʼmasiku amene akubwerawo, Yakobo adzamera mizu,

      Isiraeli adzaphuka nʼkuchita maluwa,+

      Ndipo iwo adzadzaza dzikolo ndi zipatso.+

  • Yesaya 35:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  6 Pa nthawi imeneyo, munthu wolumala adzadumpha ngati mmene imachitira mbawala,+

      Ndipo lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mosangalala.+

      Mʼchipululu mudzatumphuka madzi,

      Ndipo mʼdera lachipululu mudzayenda mitsinje.

  • Yesaya 51:3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  3 Chifukwa Yehova adzatonthoza Ziyoni.+

      Iye adzatonthoza malo ake onse amene anawonongedwa.+

      Adzachititsa chipululu chake kukhala ngati Edeni+

      Ndipo dera lake lachipululu lidzakhala ngati munda wa Yehova.+

      Mwa iye mudzakhala kusangalala ndi kukondwera,

      Kuyamikira ndi kuimba nyimbo zosangalatsa.+

  • Ezekieli 36:35
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 35 Anthu adzanena kuti: “Dziko limene linali bwinja tsopano lakhala ngati munda wa Edeni.+ Mizinda imene inawonongedwa ija, imene inali mabwinja ndiponso imene nyumba zake zinagwetsedwa, tsopano ili ndi mipanda yolimba kwambiri ndipo mukukhala anthu.”+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena