Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mafumu 18:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Mʼchaka cha 14 cha Mfumu Hezekiya, Senakeribu mfumu ya Asuri+ anabwera kudzaukira mizinda yonse ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri ndipo analanda mizindayo.+

  • 2 Mbiri 32:1
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 32 Pambuyo pa zimenezi ndiponso pambuyo pa zinthu zokhulupirika+ zimene Hezekiya anachitazi, Senakeribu mfumu ya Asuri anabwera kuti adzaukire Yuda. Iye anamanga misasa pafupi ndi mizinda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri nʼcholinga choti alowe nʼkulanda mizindayo.+

  • Yesaya 8:7, 8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  7 Yehova adzawabweretsera

      madzi ambiri komanso amphamvu a mu Mtsinje*

      Omwe ndi mfumu ya Asuri+ ndi ulemerero wake wonse.

      Mfumuyo idzadzaza timitsinje take tonse

      Nʼkusefukira mʼmphepete mwake monse

       8 Ndipo idzakokolola chilichonse mu Yuda.

      Idzadutsa nʼkusefukira, moti idzafika mpaka mʼkhosi.+

      Idzatambasula mapiko ake mpaka mʼlifupi mwa dziko lako,

      Iwe Emanueli.”*+

  • Yesaya 10:28-32
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Iye wafika ku Ayati.+

      Wadutsa ku Migironi.

      Ndipo katundu wake wamuika ku Mikimasi.+

      29 Iwo adutsa powolokera mtsinje.

      Usiku agona ku Geba.+

      Rama wanjenjemera ndipo Gibeya,+ kwawo kwa Sauli, wathawa.+

      30 Iwe mwana wamkazi wa Galimu, lira ndi kufuula kwambiri.

      Khala tcheru iwe Laisa,

      Iwenso Anatoti womvetsa chisoni!+

      31 Madimena wathawa.

      Anthu okhala ku Gebimu abisala.

      32 Tsiku lomwelo iye akaima ku Nobu.+

      Iye akuopseza ndi chibakera phiri la mwana wamkazi wa Ziyoni,*

      Phiri limene pali Yerusalemu.

  • Yesaya 33:8
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    •  8 Mʼmisewu ikuluikulu mulibe aliyense.

      Palibe munthu aliyense amene akuyenda mʼnjira.

      Iye* waphwanya pangano,

      Wakana mizinda

      Ndipo sakusamala za munthu aliyense.+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena