-
2 Mbiri 32:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Musalole kuti Hezekiya akupusitseni kapena kukusocheretsani chonchi.+ Musamukhulupirire, chifukwa palibe mulungu wa ufumu uliwonse kapena wa mtundu uliwonse amene anatha kupulumutsa anthu ake mʼmanja mwanga ndiponso mʼmanja mwa makolo anga akale. Ndiye mukuganiza kuti Mulungu wanu angakupulumutseni mʼmanja mwanga?’”+
-
-
Danieli 3:15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Ndiye ngati ndinu okonzeka kugwada nʼkulambira fano lagolide, mukamva kulira kwa lipenga, chitoliro, zeze wamngʼono, zeze wamakona atatu, choimbira chazingwe, chitoliro chathumba ndi zipangizo zina zonse zoimbira, zili bwino. Koma mukakana kulambira, nthawi yomweyo muponyedwa mungʼanjo yoyaka moto. Ndipo ndi mulungu uti amene angakupulumutseni mʼmanja mwanga?”+
-