-
Yeremiya 40:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Ndiye Ayuda onse amene anali ku Mowabu, ku Amoni, ku Edomu komanso amene anali mʼmayiko ena onse anamvanso kuti mfumu ya Babulo yalola kuti anthu amene anatsala azikhala ku Yuda komanso kuti yaika Gedaliya mwana wa Ahikamu mwana wa Safani kuti aziwalamulira. 12 Choncho Ayuda onse anayamba kubwerera kuchokera kumadera onse kumene anawabalalitsira ndipo anabwera mʼdziko la Yuda kwa Gedaliya ku Mizipa. Iwo anasonkhanitsa vinyo ndi zipatso zamʼchilimwe zochuluka kwambiri.
-