11 Pamenepo Ayuda onse amene anali kukhala ku Mowabu, amenenso anali kukhala pakati pa ana a Amoni, amene anali ku Edomu ndi ena amene anali m’mayiko ena onse+ anamva kuti mfumu ya Babulo yaika Gedaliya+ mwana wa Ahikamu mwana wa Safani kukhala wolamulira anthu otsala ku Yuda.