4 mudzanena mwambi uwu wonyoza mfumu ya Babulo:
“Amene ankagwiritsa ntchito anzake mokakamiza uja wawonongedwa!
Kuponderezedwa kuja kwatha ndithu!+
5 Yehova wathyola ndodo ya anthu oipa,
Ndodo ya anthu olamulira.+
6 Wathyola ndodo ya amene ankakwapula mwaukali komanso mosalekeza anthu a mitundu ina,+
Amene anagonjetsa mitundu ya anthu mokwiya powazunza mosalekeza.+