Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Ekisodo 32:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Kumbukirani Abulahamu, Isaki ndi Isiraeli atumiki anu, amene munawalumbirira powauza kuti: ‘Ndidzachulukitsa mbadwa* zanu ngati nyenyezi zakumwamba+ ndipo dziko lonseli limene ndinalisankha, ndidzalipereka kwa mbadwa* zanu, kuti likhale lawo mpaka kalekale.’”+

  • Levitiko 26:41, 42
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 41 Atatero, inenso ndinayenda motsutsana nawo+ ndipo ndinawapititsa kudziko la adani awo.+

      Izi zinachitika kuti mwina mitima yawo yosadulidwayo ingadzichepetse+ nʼkulipira chifukwa cha zolakwa zawo. 42 Choncho ndidzakumbukira pangano limene ndinachita ndi Yakobo,+ Isaki+ komanso Abulahamu.+ Ndidzakumbukiranso dzikolo.

  • Salimo 106:43-45
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 43 Nthawi zambiri ankawapulumutsa,+

      Koma iwo ankamupandukira komanso sankamvera,+

      Ndipo ankawonongedwa chifukwa cha zolakwa zawo.+

      44 Koma Mulungu ankaona mavuto amene akukumana nawo+

      Ndipo ankamva kulira kwawo kopempha thandizo.+

      45 Pofuna kuwathandiza iye ankakumbukira pangano lake,

      Ndipo ankawamvera chisoni* chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika chomwe ndi chachikulu.*+

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena