-
Numeri 18:26, 27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 “Uza Alevi kuti, ‘Muzilandira kwa Aisiraeli chakhumi chimene ndakupatsani kuti chikhale cholowa chanu.+ Ndipo pa chakhumi chimene muzilandiracho, muzipereka chakhumi kwa Yehova.+ 27 Chakhumicho Mulungu azichiona kuti ndi chopereka chanu mofanana ndi tirigu wochokera pamalo opunthira,+ vinyo wochuluka wochokera mopondera mphesa kapena mafuta ochuluka ochokera mʼchofinyira mafuta.
-