8 Pa nthawi imene ndimayangʼanitsitsa nyangazo, ndinaona kuti nyanga ina yaingʼono+ yamera pakati pa nyangazo. Nyanga zitatu pa nyangazi zinazulidwa pamalo amene nyanga yaingʼonoyo inamera. Nyangayi inali ndi maso ngati a munthu, ndipo inali ndi pakamwa polankhula mawu odzitukumula.+