8 Pamene ndinali kuyang’anitsitsa nyangazo, ndinaona kuti nyanga ina yaing’ono yamera+ pakati pa nyangazo. Nyanga zitatu pa nyangazi zinazulidwa pamalo amene nyanga yaing’onoyo inamera. Nyangayi inali ndi maso ngati a munthu, ndipo inali ndi pakamwa polankhula mawu odzitukumula.+