Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mbiri 36:20, 21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Nebukadinezara anatenga anthu amene sanaphedwe ndi lupanga+ nʼkupita nawo ku Babulo. Anthuwo anakhala antchito ake+ ndiponso a ana ake mpaka pamene ufumu wa Perisiya unayamba kulamulira.+ 21 Zimenezi zinachitika pokwaniritsa mawu a Yehova amene ananena kudzera mwa Yeremiya,+ mpaka pamene dzikolo linalipira masabata ake.+ Masiku onse amene dzikolo linali bwinja linkasunga sabata mpaka zinakwana zaka 70.+

  • Yeremiya 25:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Dziko lonseli lidzakhala bwinja ndipo lidzakhala chinthu chochititsa mantha. Mitundu imeneyi idzatumikira mfumu ya ku Babulo zaka 70.”’+

  • Yeremiya 29:10
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 10 “Yehova wanena kuti, ‘Zaka 70 zikadzakwana muli ku Babulo, ndidzakusamalirani+ ndipo ndidzakwaniritsa lonjezo langa pokubwezeretsani kumalo ano.’+

  • Zekariya 1:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Choncho mngelo wa Yehova anati: “Inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, kodi Yerusalemu ndiponso mizinda ya Yuda+ imene munaikwiyira kwa zaka 70 zimenezi,+ simuichitira chifundo mpaka liti?”

  • Zekariya 7:5
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 5 “Kauze anthu onse amʼdzikoli ndi ansembe kuti, ‘Pamene munkasala kudya ndi kulira mʼmwezi wa 5 komanso mʼmwezi wa 7+ kwa zaka 70,+ kodi munkasaladi kudya chifukwa cha ine?

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena