Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • 2 Mbiri 36:20, 21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 20 Nebukadinezara anatenga anthu amene sanaphedwe ndi lupanga+ nʼkupita nawo ku Babulo. Anthuwo anakhala antchito ake+ ndiponso a ana ake mpaka pamene ufumu wa Perisiya unayamba kulamulira.+ 21 Zimenezi zinachitika pokwaniritsa mawu a Yehova amene ananena kudzera mwa Yeremiya,+ mpaka pamene dzikolo linalipira masabata ake.+ Masiku onse amene dzikolo linali bwinja linkasunga sabata mpaka zinakwana zaka 70.+

  • Ezara 1:1-3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 1 Mʼchaka choyamba cha Koresi+ mfumu ya Perisiya, pokwaniritsa mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa Yeremiya,+ Yehova analimbikitsa Koresi mfumu ya Perisiya kuti alengeze mu ufumu wake wonse, zomwenso iye analemba mʼmakalata,+ kuti:

      2 “Koresi mfumu ya Perisiya wanena kuti, ‘Yehova Mulungu wakumwamba wandipatsa maufumu onse apadziko lapansi.+ Iye wandituma kuti ndimumangire nyumba ku Yerusalemu+ mʼdziko la Yuda. 3 Aliyense amene ali pakati panu mwa anthu onse amene amamutumikira, Mulungu wake akhale naye ndipo apite ku Yerusalemu mʼdziko la Yuda nʼkukamanganso nyumba ya Yehova Mulungu wa Isiraeli. Iye ndi Mulungu woona ndipo nyumba yake inali ku Yerusalemu.*

  • Danieli 9:2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 mʼchaka choyamba cha ulamuliro wake, ineyo Danieli ndinazindikira chiwerengero cha zaka zimene zinatchulidwa mʼmawu amene Yehova anauza mneneri Yeremiya, kuti Yerusalemu adzakhala bwinja+ kwa zaka 70.+ Ndinazindikira zimenezi nditawerenga mʼmabuku.*

  • Zekariya 1:12
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 12 Choncho mngelo wa Yehova anati: “Inu Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, kodi Yerusalemu ndiponso mizinda ya Yuda+ imene munaikwiyira kwa zaka 70 zimenezi,+ simuichitira chifundo mpaka liti?”

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena