-
Danieli 2:40-42Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
40 Ufumu wa nambala 4 udzakhala wolimba ngati chitsulo.+ Mofanana ndi chitsulo chimene chimaphwanya nʼkupera china chilichonse, ufumuwo udzaphwanya nʼkuwonongeratu maufumu ena onsewa.+
41 Mogwirizana ndi zimene munaona kuti mapazi ndi zala zakumiyendo zinali zadongo la woumba mbiya losakanikirana ndi chitsulo, ufumuwo udzakhala wogawanika. Koma udzakhala wolimba pa zinthu zina ngati chitsulo, ngati mmene munaonera kuti chitsulocho chinali chosakanikirana ndi dongo lofewa. 42 Popeza zala zakumiyendo zinali zachitsulo chosakanikirana ndi dongo, pa zinthu zina ufumuwo udzakhala wolimba koma pa zinthu zina udzakhala wosalimba.
-