-
Danieli 5:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Mu ufumu wanu muli munthu amene ali ndi mzimu wa milungu yoyera. Mʼmasiku a bambo anu, anthu anazindikira kuti munthuyu ndi wodziwa zinthu kwambiri, wozindikira ndiponso ali ndi nzeru zofanana ndi nzeru za milungu.+ Ndiyeno bambo anu, Mfumu Nebukadinezara, anamuika kuti akhale mkulu wa ansembe ochita zamatsenga, anthu okhulupirira mizimu, Akasidi* ndi anthu okhulupirira nyenyezi.+ Ndithudi mfumu, bambo anu anamupatsa udindo umenewu. 12 Anachita zimenezi chifukwa Danieli, amene mfumu inamupatsa dzina lakuti Belitesazara,+ anali ndi luso lodabwitsa, anali wodziwa zinthu ndi wozindikira pa nkhani yomasulira maloto, kumasulira mikuluwiko komanso kuthana ndi zinthu zovuta.*+ Tsopano itanani Danieli ndipo akuuzani kumasulira kwa mawu amenewa.”
-