4 Koma mfumu ya Asuri inamva kuti Hoshiya akuikonzera chiwembu, chifukwa anatumiza anthu kwa So mfumu ya Iguputo+ ndiponso sanapereke msonkho kwa mfumu ya Asuri ngati mmene ankachitira zaka zamʼmbuyo. Choncho mfumu ya Asuri inamʼmanga nʼkumutsekera mʼndende.