-
Mateyu 12:39, 40Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
39 Poyankha iye anawauza kuti: “Mʼbadwo woipa komanso wachigololo* ukufunitsitsa utaona chizindikiro. Koma sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse kupatulapo chizindikiro cha mneneri Yona chokha.+ 40 Chifukwa mofanana ndi Yona amene anakhala mʼmimba mwa chinsomba chachikulu masiku atatu, masana ndi usiku,+ Mwana wa munthu nayenso adzakhala mumtima wa dziko lapansi masiku atatu, masana ndi usiku.+
-
-
Luka 11:29, 30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Pamene gulu la anthulo linkachulukirachulukira, iye anayamba kunena kuti: “Mʼbadwo uwu ndi mʼbadwo woipa, ukufuna chizindikiro. Koma sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse kupatulapo chizindikiro cha Yona chokha.+ 30 Mofanana ndi Yona+ amene anakhala chizindikiro kwa anthu a ku Nineve, Mwana wa munthu adzakhalanso chizindikiro ku mʼbadwo uwu.
-