Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • Levitiko 7:21
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 21 Munthu akakhudza chilichonse chodetsedwa, kaya ndi chodetsa chochokera kwa munthu+ kapena nyama yodetsedwa,+ kapenanso chinthu chilichonse chonyansa chodetsedwa,+ nʼkudya ina mwa nyama ya nsembe yamgwirizano, imene ndi ya Yehova, munthu ameneyo aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.’”

  • Numeri 5:2, 3
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 2 “Lamula Aisiraeli kuti azitulutsa mumsasa munthu aliyense wakhate,+ aliyense wakukha kumaliseche+ komanso aliyense wodetsedwa chifukwa chokhudza munthu wakufa.+ 3 Kaya akhale mwamuna kapena mkazi, uziwatulutsa mumsasa kuti asadetse+ misasa ya anthu amene ine ndikukhala pakati pawo.”+

  • Numeri 9:6
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 6 Tsopano panali amuna ena amene anadzidetsa chifukwa chokhudza mtembo wamunthu,+ moti sanathe kukonza nsembe ya Pasika pa tsikulo. Choncho amunawo anakaonekera kwa Mose ndi Aroni pa tsikulo,+

  • Numeri 19:11
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 11 Aliyense wokhudza mtembo wa munthu aliyense, azikhala wodetsedwa kwa masiku 7.+

  • Numeri 31:19
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 19 Mumange msasa kunja kwa msasawu, ndipo mukhalemo masiku 7. Aliyense amene wapha munthu komanso aliyense amene wakhudza mtembo wa munthu wophedwa,+ adziyeretse+ pa tsiku lachitatu ndi pa tsiku la 7. Mudziyeretse limodzinso ndi anthu amene mwawagwirawo.

Mabuku a Chichewa (1974-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chichewa
  • Tumizirani Ena
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • Privacy Settings
  • JW.ORG
  • Lowani
Tumizirani Ena