-
Luka 19:37, 38Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
37 Atangofika pafupi ndi msewu wochokera mʼphiri la Maolivi, gulu lonse la ophunzirawo linayamba kusangalala ndi kutamanda Mulungu mokweza mawu chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu zimene anaona. 38 Iwo ankanena kuti: “Wodalitsidwa ndi amene akubwera monga Mfumu mʼdzina la Yehova!* Mtendere kumwamba ndi ulemerero kumwambamwambako!”+
-