9 “Ine ndidzatenga anthu otsalawo nʼkuwaika pamoto.
Ndipo ndidzawayenga ngati mmene amayengera siliva
Komanso kuwayesa ngati mmene amayesera golide.+
Iwo adzaitana dzina langa,
Ndipo ine ndidzawayankha.
Ndidzanena kuti, ‘Awa ndi anthu anga,’+
Ndipo iwo adzanena kuti, ‘Yehova ndi Mulungu wathu.’”