-
Maliko 1:16-18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Pamene ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya,* Yesu anaona Simoni ndi Andireya+ mchimwene wake wa Simoniyo, akuponya maukonde awo mʼnyanjamo+ chifukwa anali asodzi.+ 17 Choncho Yesu anawauza kuti: “Nditsatireni ndipo ndikusandutsani asodzi a anthu.”+ 18 Nthawi yomweyo iwo anasiya maukonde awo nʼkumutsatira.+
-