19 Atapita patsogolo pangʼono, anaona Yakobo mwana wa Zebedayo ndi mchimwene wake Yohane, ali mungalawa yawo ndipo ankasoka maukonde awo.+ 20 Nthawi yomweyo anawaitana. Choncho iwo anasiya bambo awo a Zebedayo mʼngalawamo limodzi ndi anthu aganyu ndipo anamutsatira.