21 Atadutsa pamenepo, anaona amuna enanso awiri apachibale, Yakobo mwana wa Zebedayo ndi mchimwene wake Yohane.+ Iwo anali mʼngalawa limodzi ndi bambo awo, a Zebedayo, akusoka maukonde awo, ndipo anawaitana.+ 22 Nthawi yomweyo anasiya ngalawa ija ndi bambo awo nʼkumutsatira.