-
Luka 6:47-49Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
47 Aliyense amene amabwera kwa ine kudzamva mawu anga, nʼkuchita zimene wamvazo, ndikuuzani amene amafanana naye:+ 48 Iyeyo ali ngati munthu amene pomanga nyumba, anakumba mozama kwambiri nʼkuyala maziko pathanthwe. Ndiye mtsinje utasefukira, madzi anawomba nyumbayo, koma sanathe kuigwedeza chifukwa anaimanga bwino.+ 49 Pamene munthu amene wamva koma osachita chilichonse,+ ali ngati munthu amene wamanga nyumba yopanda maziko padothi. Apanso mtsinje unasefukira nʼkuwomba nyumbayo, ndipo nthawi yomweyo inagwa, moti kugwa kwake kunali kwakukulu.”
-