Mateyu 23:34 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 34 Pa chifukwa chimenechi, ndikukutumizirani aneneri,+ anthu anzeru ndi aphunzitsi.+ Ena a iwo mudzawapha+ nʼkuwapachika pamtengo ndipo ena mudzawakwapula+ mʼmasunagoge mwanu ndi kuwazunza+ mumzinda ndi mzinda, Maliko 13:9 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 9 Koma inu khalani ochenjera. Anthu adzakutengerani kumakhoti aangʼono+ ndipo adzakukwapulani mumasunagoge+ nʼkukuimikani pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu chifukwa ndinu otsatira anga, kuti iwowo aphunzire za ine.+ Luka 21:12, 13 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 12 Koma zinthu zonsezi zisanachitike, anthu adzakugwirani nʼkukuzunzani+ ndipo adzakuperekani kumasunagoge ndi kundende. Adzakupititsani kwa mafumu ndi abwanamkubwa chifukwa cha dzina langa.+ 13 Zimenezi zidzakupatsani mpata woti muchitire umboni.
34 Pa chifukwa chimenechi, ndikukutumizirani aneneri,+ anthu anzeru ndi aphunzitsi.+ Ena a iwo mudzawapha+ nʼkuwapachika pamtengo ndipo ena mudzawakwapula+ mʼmasunagoge mwanu ndi kuwazunza+ mumzinda ndi mzinda,
9 Koma inu khalani ochenjera. Anthu adzakutengerani kumakhoti aangʼono+ ndipo adzakukwapulani mumasunagoge+ nʼkukuimikani pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu chifukwa ndinu otsatira anga, kuti iwowo aphunzire za ine.+
12 Koma zinthu zonsezi zisanachitike, anthu adzakugwirani nʼkukuzunzani+ ndipo adzakuperekani kumasunagoge ndi kundende. Adzakupititsani kwa mafumu ndi abwanamkubwa chifukwa cha dzina langa.+ 13 Zimenezi zidzakupatsani mpata woti muchitire umboni.