-
Luka 7:24-28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Anthu amene Yohane anawatuma aja atachoka, Yesu anayamba kuuza gulu la anthu za Yohane kuti: “Kodi munapita mʼchipululu kukaona chiyani? Kodi munapita kukaona bango logwedezeka ndi mphepo?+ 25 Nanga munapita kukaona chiyani? Munthu wovala zovala zapamwamba kapena?+ Ayi, paja amene amavala zovala zapamwamba ndiponso anthu amene amakhala moyo wamwanaalirenji amapezeka mʼnyumba zachifumu. 26 Nangano munapita kukaona chiyani makamaka? Mneneri kapena? Inde, ndikukuuzani, Yohane ndi mneneri komanso ndi wofunika kwambiri kuposa aneneri.+ 27 Malemba amanena za iyeyu kuti: ‘Taona! Inetu ndikutumiza mthenga wanga kuti atsogole kukakukonzera njira.’+ 28 Ndithudi ndikukuuzani, pa anthu onse,* palibe wamkulu kuposa Yohane. Koma munthu amene ali wocheperapo mu Ufumu wa Mulungu ndi wamkulu kuposa iyeyu.”+
-