-
1 Akorinto 2:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Koma mogwirizana ndi zimene Malemba amanena: “Palibe munthu amene anaonapo kapena kumva kapenanso kuganiza zimene Mulungu wakonzera anthu amene amamukonda.”+ 10 Mulungu anatiululira ifeyo zinthu zimenezi+ kudzera mwa mzimu wake,+ chifukwa mzimu umafufuza zinthu zonse, ngakhale zinthu zozama za Mulungu.+
-
-
Aefeso 1:9-12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 potiululira chinsinsi chake chopatulika+ chokhudza chifuniro chake. Chinsinsicho nʼchogwirizana ndi zimene zimamusangalatsa ndiponso zimene amafuna, 10 zoti akakhazikitse dongosolo lake pa nthawi imene anaikiratu. Dongosolo limenelo ndi kusonkhanitsa zinthu zonse pamodzi kuti zikhale zogwirizana ndi Khristu, zinthu zakumwamba ndi zinthu zapadziko lapansi.+ Inde, zinthu zonse zidzasonkhanitsidwa kwa Khristu, 11 amene chifukwa chogwirizana naye tinasankhidwa kuti tidzalandire cholowa,+ chifukwa anatisankha kale mwa kufuna kwake, iye amene amachita zinthu zonse mogwirizana ndi chifuniro chake. 12 Anachita zimenezo kuti ifeyo amene ndife oyamba kukhala ndi chiyembekezo mwa Khristu titamande Mulungu chifukwa iye ndi wamkulu.
-
-
Akolose 1:26, 27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Mawuwo akuphatikizapo chinsinsi chopatulika+ chimene dziko silinachidziwe+ ndiponso chinali chobisika kwa mibadwo yakale. Koma tsopano chaululidwa kwa oyera ake.+ 27 Mulungu zinamusangalatsa kuululira oyera pakati pa anthu a mitundu ina chinsinsi chopatulikachi,+ chomwe chili ndi ulemerero wochuluka komanso chuma chauzimu. Chinsinsi chimenechi ndi Khristu amene ndi wogwirizana ndi inuyo, kutanthauza kuti muli ndi chiyembekezo chodzalandira ulemerero limodzi ndi Khristuyo.+
-