27 Mulungu anaululira anthu a mitundu ina chinsinsi chopatulikachi,+ chimene chili chodzaza ndi ulemerero ndi chuma chauzimu.+ Chinsinsicho n’chakuti Khristu+ ndi wogwirizana ndi inuyo, zimene zikutanthauza kuti muli ndi chiyembekezo chodzalandira ulemerero pamodzi naye.+