-
Luka 4:1-4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Kenako Yesu anachoka ku Yorodano atadzazidwa ndi mzimu woyera ndipo mzimuwo unamutenga nʼkumuyendetsa malo osiyanasiyana mʼchipululu+ 2 kwa masiku 40, kumene ankayesedwa ndi Mdyerekezi.+ Pa masiku amenewo sanadye chilichonse ndipo masikuwo atatha, anamva njala. 3 Mdyerekezi ataona zimenezi anamuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu kuti usanduke mkate.” 4 Koma Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amati, ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha.’”+
-