35 Ena mwa anthu amene anaimirira chapafupi atamva zimenezo anayamba kunena kuti: “Tamverani! Akuitana Eliya.” 36 Kenako wina anathamanga kukaviika siponji muvinyo wowawasa ndipo anaiika kubango nʼkumupatsa kuti amwe.+ Iye ananena kuti: “Mulekeni! Tione ngati Eliya angabwere kudzamutsitsa.”