19 Ndiyeno popeza kuti Yohane anadzudzula Herode wolamulira chigawo pa nkhani yokhudza Herodiya, mkazi wa mʼbale wake, komanso chifukwa cha zoipa zonse zimene Herode anachita, 20 Herode anawonjezera choipa china pa zonsezo: Anatsekera Yohane mʼndende.+