-
Mateyu 14:3-5Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Herode* anagwira Yohane nʼkumumanga ndipo anamutsekera mʼndende chifukwa cha Herodiya, mkazi wa mchimwene wake Filipo amene Herodeyo anakwatira.+ 4 Anachita zimenezi chifukwa Yohane ankamuuza kuti: “Nʼzosaloleka kuti mutenge mkazi ameneyu kukhala mkazi wanu.”+ 5 Komabe, ngakhale kuti Herode ankafuna kupha Yohane, ankaopa gulu la anthu chifukwa iwo ankakhulupirira kuti anali mneneri.+
-
-
Maliko 6:17-20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Ananena zimenezi chifukwa Herodeyo anatumiza anthu kuti akagwire Yohane nʼkumumanga ndipo anamutsekera mʼndende chifukwa cha Herodiya, mkazi wa mchimwene wake Filipo amene Herodeyo anakwatira.+ 18 Anachita zimenezi chifukwa Yohane ankauza Herode kuti: “Nʼzosaloleka kuti mutenge mkazi wa mchimwene wanu.”+ 19 Choncho Herodiya anamusungira chidani mumtima ndipo ankafuna kumupha, koma sanakwanitse kuchita zimenezo. 20 Herode ankaopa Yohane chifukwa ankadziwa kuti ndi munthu wolungama komanso woyera,+ choncho ankamuteteza. Atamva zimene ankanena anathedwa nzeru, komabe anapitiriza kumumvetsera mosangalala.
-