-
2 Mafumu 4:42-44Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
42 Ndiyeno kunabwera munthu wina kuchokera ku Baala-salisa.+ Iye anabweretsera munthu wa Mulungu woonayo mikate 20 ya balere+ woyambirira kucha komanso thumba la tirigu* watsopano.+ Kenako Elisa anati: “Apatse anthuwa kuti adye.” 43 Koma mtumiki wakeyo anati: “Ndingagawire bwanji anthu 100 chakudya chimenechi?”+ Elisa anati: “Agawire anthuwa kuti adye chifukwa Yehova wanena kuti, ‘Anthu adya nʼkukhuta ndipo china chitsala.’”+ 44 Atamva zimenezi, anagawira anthuwo chakudyacho. Iwo anadya ndipo china chinatsala+ mogwirizana ndi mawu a Yehova.
-