-
Mateyu 15:3-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Koma iye anawayankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani inuyo mumaphwanya malamulo a Mulungu chifukwa cha miyambo yanu?+ 4 Mwachitsanzo, Mulungu ananena kuti, ‘Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu.’+ Komanso anati, ‘Aliyense wolankhula mawu achipongwe kwa bambo ake kapena mayi ake aziphedwa.’+ 5 Koma inu mumanena kuti, ‘Aliyense wouza bambo ake kapena mayi ake kuti: “Chilichonse chimene ndili nacho, chimene ndikanakuthandizani nacho ndi mphatso yoti ndipereke kwa Mulungu,”+ 6 sakuyenera kuthandiza bambo ake.’ Choncho mwachititsa kuti mawu a Mulungu akhale opanda pake chifukwa cha miyambo yanu.+
-