-
Maliko 7:8-13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Mumanyalanyaza malamulo a Mulungu nʼkumaumirira miyambo ya anthu.”+
9 Komanso anawauza kuti: “Mochenjera, mumanyalanyaza malamulo a Mulungu kuti musunge miyambo yanu.+ 10 Mwachitsanzo, Mose ananena kuti, ‘Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu,’+ komanso anati, ‘Aliyense wolankhula mawu achipongwe kwa bambo ake kapena mayi ake aziphedwa.’+ 11 Koma inu mumanena kuti, ‘Munthu akauza bambo ake kapena mayi ake kuti: “Chilichonse chimene ndili nacho, chimene ndikanakuthandizani nacho ndi khobani (kutanthauza, mphatso yoti ndipereke kwa Mulungu),”’ 12 inu simulolanso kuti munthuyo achitire bambo ake kapena mayi ake chinthu chilichonse.+ 13 Mukamachita zimenezi, mumapangitsa kuti mawu a Mulungu akhale opanda pake chifukwa cha miyambo yanu imene munaipereka kwa anthu.+ Ndipo mumachita zinthu zambiri ngati zimenezi.”+
-