41 Ndiyeno anatenga mitanda ya mkate 5 ndi nsomba ziwiri zija nʼkuyangʼana kumwamba ndipo anapemphera.+ Kenako ananyemanyema mitanda ya mkateyo nʼkuipereka kwa ophunzira ake kuti aipereke kwa anthuwo ndiponso anaduladula nsomba ziwirizo nʼkugawira anthu onsewo.