Mateyu 14:23 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 23 Atauza anthuwo kuti azipita, anakwera phiri yekhayekha kukapemphera.+ Iye anakhala kumeneko yekhayekha mpaka kunja kunada. Maliko 14:32 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 32 Kenako anafika pamalo otchedwa Getsemane ndipo anauza ophunzira akewo kuti: “Khalani pansi panopa, ine ndikukapemphera.”+ Luka 4:42 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 42 Kutacha, anachoka nʼkupita kumalo kopanda anthu.+ Koma gulu la anthu linayamba kumufunafuna mpaka linafika kumene iye anali, ndipo anthuwo anamupempha kuti asachoke. Aheberi 5:7 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 7 Pamene Khristu anali padzikoli,* anapereka mapemphero ochonderera ndiponso opempha, kwa amene akanatha kumupulumutsa ku imfa. Anapereka mapempherowa mofuula komanso akugwetsa misozi,+ ndipo anamumvera chifukwa ankaopa Mulungu.
23 Atauza anthuwo kuti azipita, anakwera phiri yekhayekha kukapemphera.+ Iye anakhala kumeneko yekhayekha mpaka kunja kunada.
32 Kenako anafika pamalo otchedwa Getsemane ndipo anauza ophunzira akewo kuti: “Khalani pansi panopa, ine ndikukapemphera.”+
42 Kutacha, anachoka nʼkupita kumalo kopanda anthu.+ Koma gulu la anthu linayamba kumufunafuna mpaka linafika kumene iye anali, ndipo anthuwo anamupempha kuti asachoke.
7 Pamene Khristu anali padzikoli,* anapereka mapemphero ochonderera ndiponso opempha, kwa amene akanatha kumupulumutsa ku imfa. Anapereka mapempherowa mofuula komanso akugwetsa misozi,+ ndipo anamumvera chifukwa ankaopa Mulungu.