-
Mateyu 12:9-14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Atachoka malo amenewo, anakalowa musunagoge wawo. 10 Mmenemo munali munthu wolumala dzanja.+ Choncho iwo anamufunsa kuti, “Kodi nʼzololeka kuchiritsa odwala pa tsiku la Sabata?” Cholinga chawo chinali choti amupezere chifukwa nʼkumuimba mlandu.+ 11 Koma iye anawayankha kuti: “Mutakhala ndi nkhosa imodzi yokha, ndiyeno nkhosayo nʼkugwera mʼdzenje pa tsiku la Sabata, kodi alipo pakati panu amene sangaigwire nʼkuitulutsa?+ 12 Komatu munthu ndi wofunika kwambiri kuposa nkhosa! Choncho ndi zololeka kuchita chinthu chabwino pa tsiku la Sabata.” 13 Kenako anauza munthuyo kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi ndipo linakhalanso bwinobwino ngati linzake. 14 Koma Afarisiwo anatuluka nʼkukakonza chiwembu kuti amuphe.
-
-
Maliko 3:1-6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
3 Kachiwirinso Yesu analowa musunagoge. Mmenemo munali munthu wolumala dzanja.+ 2 Ndiyeno Afarisi ankamuyangʼanitsitsa kuti aone ngati angachiritse munthuyo pa Sabata nʼcholinga choti amuimbe mlandu. 3 Ndipo iye anauza munthu wolumala dzanjayo kuti: “Nyamuka, bwera pakatipa.” 4 Kenako anawafunsa kuti: “Kodi malamulo amalola kuchita chiyani pa Sabata, chabwino kapena choipa? Kupulumutsa moyo kapena kupha?”+ Koma iwo anangokhala chete. 5 Yesu anawayangʼana mokwiya ndipo anamva chisoni kwambiri chifukwa cha kuuma mtima kwawo.+ Kenako anauza munthuyo kuti: “Tambasula dzanja lako.” Iye analitambasuladi ndipo linakhala labwinobwino. 6 Ataona zimenezi Afarisiwo anatuluka ndipo nthawi yomweyo anapita kukakonza chiwembu limodzi ndi anthu amene ankatsatira Herode+ kuti amuphe.
-