-
Mateyu 1:21-23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Iye adzabereka mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina lakuti Yesu,*+ chifukwa adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.”+ 22 Zonsezi zinachitikadi kuti zimene Yehova* ananena kudzera mwa mneneri wake zikwaniritsidwe. Iye anati: 23 “Tamverani! Namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo adzamʼpatsa dzina lakuti Emanueli,”+ limene akalimasulira limatanthauza kuti “Mulungu Ali Nafe.”+
-