-
Mateyu 1:20, 21Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Koma ataganizira mozama za nkhani imeneyi, mngelo wa Yehova* anamuonekera mʼmaloto nʼkumuuza kuti: “Yosefe, mwana wa Davide, usaope kutenga Mariya mkazi wako nʼkupita naye kunyumba, popeza iye ndi woyembekezera chifukwa cha mphamvu ya mzimu woyera.+ 21 Iye adzabereka mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina lakuti Yesu,*+ chifukwa adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.”+
-